Chidziwitso: Nthata za maso a nkhuku zofiira
Mwina mukufuna kudziwa za utitiri wa nkhuku
M'Chizungu timati "stick-fast flea". Zimaoneka chonchi:
Maonekedwe a Matendawa:
- Zizindikiro: Nthawi zambiri nthata izi zimawoneka ngati mzere wakuda pamwamba pa maso. Nthawi zina, zimakhala paliponse pa mutu, kapena pena pa thupi la nkhuku. Zimakhala zokhazikika pakhungu, osayendayenda. Ngati zimayendayenda, zomwe ndi mtundu wina wa tizilombo, osati nthata za maso a nkhuku zofiira.
- Zimayamwa magazi a nkhuku, ndipo nkhukuzo zimafooka. Zina zikhoza kufa koma zochepa.
Kuchiza:
- Pakani mafuta monga Vaseline pamene pali nthata kuti zilephera kupuma ndipo zidzafa. Koma sizidzagwa kwa masiku angapo. Izi zilibe kanthu.
- Thandizani nkhuku zonse zomwe zakhudzidwa makamaka zazikulu.
- Komanso thirani mankhwala monga Actellic kapena Akheri powder pansi mkati mwa khola.
Chitaninso pakadutsa milungu itatu kapena inayi kuti muphe nthata zomwe zangotuluka kumene.
Kupewa:
- Musaiwale kuthira mankhwala pansi m'khola.
- Mphutsi za nthata izi zimakumba m'nthaka kuti zibereke. Ngati sizingathe kukumba, sizingathe kubereka.
Ngati pansi pali simenti yolimba, choncho nthata sizingathe kuberekana.
- Musabweretse nkhuku zomwe zili ndi nthata m'khola mwanu.