Chidziwitso: Za katemera wa chitopa cha nkhuku: Mtundu wa I-2

ndv01.png

Mawu awa alembedwa ndi Rural Poultry Centre m'Malawi ndi cholinga chothandiza opereka katemera mumadera. Ngati mufune kudziwa zambiri, chonde funsani ofesi ya zaulimi imene muli nayo pafupi kapena funsani ife.

Cholinga cha Katemerayu:

 • Katemerayu ndi woteteza nkhuku ku chitopa (kapena chideru).
 • Ngati nkhuku sizinatetezedwe ku chitopa pogwiritsa katemera, zambiri zimafa.
 • Koma ngati zalandira katemera kale, zochepa ndi zimene zimafa.
 • Chitetezocho chokera kukatemerayu chimayamba kugwira ntchito patatha sabata imodzi kuchokera tsiku lotemera.
 • Chitetezocho chokera kukatemera chimafooka mphamvu pang'ono pang'ono ndikutheratu mphamvu pakadutsa miyezi inayi. Nkhuku ziyenera kulandiranso katemera wina kuti chitetezo chilimbitsidwe.
 • Katemerayu ndi woteteza ku chitopa basi. Sangathe kuteteza nkhuku ku matenda ena.
 • Katemerayu ndi wopeleka chitetezo osati kuchiza. Katemerayu sangathe kuchiza nkhuku zodwala kale ndi chitopa.

Kasungidwe:

 • Katemerayu asasiyidwe pa dzuwa ngakhale kwa nthawi yochepa.
 • Katemerayu asaumitsidwe ndi kuzizira kwambiri.
 • Katemera asungidwe mu firiji kapena bokosi lozizira ndi miyala ya madzi.
 • Katemera agwiritsidwe ntchito pasanadutse masiku awiri chimuchotsereni mu firiji.
 • Katemera asungidwe pa malo ozizira.
 • Njira yabwino kuyendetsa katemerayu ndi kuika mu nsaru yonyowetsedwa ndi madzi, mkati mwa basiketi.

Kutha Mphamvu:

 • Werengani mofatsa pa botolo lakatemera, makamaka tsiku lotha mphamvu.
ndv02.png

Kagwiritsidwe Ntchito:

 • Khutchumulani botolo lakatemera musanagwiritse ntchito.
 • Donthezani kamodzi mu diso limodzi la nkhuku iliyonse. Kodonthezera kasakhudze nkhukuyo.
 • Sankhani malo a mthunzi popereka katemera. Nkhuku zonse pakholapo zilandire katemera ngakhale zogogomola kumene.
 • Sungani ma lekodi akatemera pa fomu laperekedwa kapena mu bukhu.
 • Osatemera nkhuku zodwala kale. Mwini wake adzakusambirani m'manja zikafa.

Dziwani izi:

 • Palibe chobvuta chilichonse cho chokera ku katemerayu. Katemerayu sangadwalitse munthu kapena nkhuku. Katemerayu sasokoneza mazila kapena nyama ya nkhuku m'njira iliyonse.
 • Nkhuku zomwe zimafa zitatemeredwa zimakhala zitafa ndi matenda ena kapena kuti zinali kale ndi chitopa polandira katemerayo.
pic07_20181113_101534_85pc240px.jpg
A little story
about our impact


small_p1050707.jpg
A quarter million chickens
and counting...


ndv-ns-results3.png
Does I-2 really work?
Yes, and here's how...


Facebook