Chidziwitso cha Matenda a Mthomba ya Nkhuku (Chikwirikwiti)
Matenda awa amapezeka kwambiri muno m'Malawi. Ndipo amafala kuchokera ku nkhuku zodwala pamene zakhudzana ndi zamoyo.
Photo: Trufosa Phiri
(Facebook - Local Chicken Farmers in Malawi)
Maonekedwe a Matendawa
- Zizindikiro: Tizilonda totupa pa lipombo ndi m'matende. Nthawi zina timaoneka pali ponse pa mutu.
- Nkhuku imadwala matendawa kwa sabata limodzi, nkhuku zina zitha kufa ndi matendawa.
Choyambitsa
- Kachirombo kamtundu wa virus kamene kamapezeka kwambiri muno m'Malawi.
Kuchiza
- Palibe mankhwala ochiza matendawa. Ngati matenda agwa m'khola, amatha okha.
- Koma kupaka mankhwala a iodine pa tizilonda kumathandiza kuchira.
Kuteteza
- Kuli katemera amene amapezeka ku veterinary shops. Katemerayu amateteza matendawa ngati sanagwe m'khola.