Chidziwitso: Alimi Ayenera Kudziwa za Matenda a Chitopa ndi Katemera wa I-2

nd-01.png

Chitopa ndi matenda oopysa zedi, amene akhoza kupewedwa pogwiritsa ntchito katemera wa I-2. Katemerayu amapezeka ku Central Veterinary Laboratory ku Lilongwe, ku ma veterinary shops, kapena kwa alangizi a boma. Katemerayu aperekedwe pakatha miyezi inayi iliyonse.

Palibe mankhwala ochiza chitopa. Chikafika chitopa pa mudzi, nkhuku zambiri zimafa, pokhapokha ngati zinalandirapo katemera kale.

Katemera sachiza chitopa, koma amatchinjiriza chitopa ku nkhuku zathu ndi kuzipatsa chitetezo asanabwere matendawa kwathu.

Katemera sagwira ntchito nthawi yomweyo. Chitetezo chimabwera pang'onopang'ono kufikira sabata, ndipo chimapitirira kuteteza nkhuku kwa miyezi inayi.

Alimi asamadikire chitopa chifike. Chifukwa akatero nkhuku zawo zidzafabe zambiri pokhapokha ngati zinalandirapo kale katemera.

Alangizi a ku midzi asapereke katemera ku nkhuku zodwala. Ngati nkhuku zikudwala, thupi lake limakhala lofooka, ndiye katemera sangathe kugwira ntchito bwino m'thupi lofooka. Ndiye nkhuku zimafabe. Ngati atemera nkhuku zodwala ndi kufa mlimi adzataya chikhulupiliro kwa alangizi. Pazifukwa izi alangizi aja asapereke katemera ku nkhuku zodwala.

Alimi adziwe kuti katemera wa chitopa ndi wa nkhuku iliyonse yaing'ono kapena yaikulu. Ngati katemera angaperekedwe kwa nkhuku zochepa, zotsalazo zifabe.

ndv.png


  Chizindikiro cha botolo la katemera chimaoneka chonchi:


Central Veterinary Laboratory Mw
I-2 Newcastle Disease Live Vaccine
300 doses Store at 4-8°C
Administer by eye drop
Batch No. 000  Exp Date: 00/0000
For animal use only

Onetsetsani kuti botolo silinatsegulidwe kale. Komanso werengeni bwino tsiku lotha ntchito la katemerayu.





logo-tropical-water-solutions.png
What is TWS?


small_p1050707.jpg
A quarter million chickens
and counting...


pic20170818_102628-225.jpg
How an Australian vaccine is helping rural communities in Africa.
Celia Grenning explains.


Facebook